"NGATI SANASOKONEKERE ATITHANDIZA KWAMBIRI" - BUNYA
Mphunzitsi watimu ya Premier Bet Dedza Dynamos, Andrew Bunya, wati kubwereranso kwa katswiri wawo womwetsa zigoli, Promise Kamwendo, kuwathandiza kwambiri koma pokhapokha ngati sanabalalike kaganizidwe.
Iye amayankhula patsogolo pa masewero atimuyi ndi Creck Sporting Club pa bwalo la Dedza loweruka masana ndipo wati Kamwendo abweretsa mpikisano wa osewera akutsogolo kwao.
"Ngati angakhale kuti sanasokonekere mu kaganizidwe ndekuti atithandiza kuonjezera osewera angapo kutsogolo kwathu ndekuti palibe zoti tili ndi uyu yekha koma wachita bwinoyo azisewera." Anatero Bunya.
Iye wati akuyembekezera kuti akhala masewero ovuta koma ayesetsa kuti adzasewere bwino ndi kupeza mipata yochuluka cholinga adzakwanitse kugoletsa chigoli mmasewerowa.
Dedza ili pa nambala yachikhumi ndi mapointsi okwana 23 pa masewero 18 omwe yasewera mu ligi ya TNM.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores