"LERO TIMENYA BLUE EAGLES, WANDERERS NDI SILVER" - MWAMADI
Mkulu wa masapota a timu ya FCB Nyasa Big Bullets, Stone Mwamadi, wati timu yake igonjetsa timu ya Blue Eagles pamodzi ndi aganyu ake a Mighty Mukuru Wanderers ndi Silver Strikers pomwe matimuwa akukumana mu ndime yotsiriza ya FDH Bank.
Iye amayankhula patsogolo pa masewerowa pabwalo la Bingu mu mzinda wa Lilongwe ndipo wati akuyembekezera zabwino kuchokera kutimuyi.
"A Yonah and a No Fear Malaya onse ati akwera Blue Eagles koma leroli liwamenyera limodzi, timenya matimu atatu a Blue Eagles, Wanderers ndi Silver pakamodzi." Anatero Stone.
Koma iye wapempha masapota atimu yake kusunga mwambo pa masewerowa popewa ziwawa ndi zachinyengo zina ngati kukhala ndi matikiti awoawo komanso kuti akavomereze zotsatira za masewerowa.
"Chitetezo ndi chokhwima ndipo tikumema Mapale kuti abwere mwaunyinji, ena akumakhala ndi matikiti awo tiwachenjeze kuti akazisiya komweko. Ziwawa sizabwino chipatala chomwecho chomwe yemwe wavulala akagon
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores