"SITIKUYANG'ANA MMENE ENA AKUCHITIRA" - MWASE
Mphunzitsi watimu ya Mighty Mukuru Wanderers, Meke Mwase, wati timu yake ikumatenga masewero aliwonse mmene akubwerera ndipo sikuyang'ana mmene matimu anzawo akuchitira.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonjetsa timu ya Kamuzu Barracks 1-0 pa bwalo la Civo ndipo wayamikira osewera ake kamba kolimbikira kuti achite bwino.
"Tasangalala tapambana, zinayambira kokonzekera anyamata amaoneka kuti akufunitsitsa kuti achite bwino nde analimbikira tinagoletsa mchigawo choyamba ndipo mipata mchigawo chachiwiri tinakanika koma bola tapeza chipambano." Anatero Mwase.
Iye anati timu yake ikudziwa kuti mchigawo chachiwiri, mpira ukhala ovuta koma walimbikitsa osewera ake kuti achilimike ndikumapambana mmasewero awo.
Timuyi ikadali pa nambala yachiwiri ndi mapointsi 38 tsopano pa masewero 18 omwe yasewera mu ligi ndipo ikutsala ndi mapointsi asanu ndi imodzi okha.
Zabwino zonse manoma fire ๐๐ค๐งก
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores