Nkhani
Bungwe la Super League of Malawi lalengeza kuti masewero omwe amayenera kukhalapo pakati pa FCB Nyasa Big Bullets ndi Creck Sporting Club lachitatuli asunthidwa kufikira mtsogolomu.
Timuyi yalengeza za nkhaniyi kudzera pa tsamba lawo la mchezo ndipo silinapereke chifukwa chenicheni chomwe chiganizochi chapangidwira.
Timu ya Bullets inasewera mu CAF champions league loweruka komwe inagonja ndi Red Arrows koma inali ikuchokera kosewera ndi Moyale Barracks mu masewero a mu FDH Bank.
Timuyi idzaseweranso lamulungu likudzali mu ndime yotsiriza ya chikho cha FDH ndi Blue Eagles ndipo kusewera ndi Creck lachitatu bwenzi kuli kupanikizika.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores