"ZINTHU ZIKUKHALA NGATI ZIKULOZERA KWA IFE" - MPONDA
Mphunzitsi watimu ya Silver Strikers, Peter Mponda, wati timu yake singanene kuti yatenga kale ligi koma khumbo la aliyense kuti chaka chino apambane ligiyi likuoneka kuti layamba kutheka.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonjetsa Mighty Tigers 2-0 pa bwalo la Silver loweruka masana ndipo wati amadziwa kuti masewero akhale ovuta poti Tigers simafuna kutsegula kumbuyo kwawo koma wayamikira anyamata ake posunga zomwe anawauza.
Iye wati padakali Pano timu yake sinapambane kalikonse ndipo sanakhutitsidwe poti ntchito ikadalipo yambiri.
"Sikuti tinganene kuti tapambana kale ligi ayi koma anyamata akutipatsa zimene tikufuna angakhale ligi isanayambe aliyense linali khumbo lake kuti tipambane ligi nde zikuoneka kuti zinthu zayamba kulozera kwa Ife." Anatero Mponda.
Timu ya Silver ikadali pa nambala yoyamba ndi mapointsi 43 pa masewero 17 omwe yasewera.
Silver
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores