"KOYAMBILIRAKU TIWASOWA KAMWENDO NDI GAMPHANI" - BUNYA
Mphunzitsi watimu ya Premier Bet Dedza Dynamos, Andrew Bunya, wati timu yawo iwasowa osewera awiri omwe achoka kutimuyi, Promise Kamwendo ndi Lameck Gamphani, koma koyambiliraku poti sangawabwenzeretse ka nthawi kochepa.
Iye amayankhula patsogolo pa masewero awo ndi Bangwe All Stars pa bwalo la Balaka loweruka ndipo wati osewera omwe alipowo sangathe kufikira pa mulingo wa awiriwa koma akawaphunzitsabe akhala abwino.
"Tikamasewera chonchi anyamata ena amatha kuwala ndi amatha kutichokera nde tiwafunire zabwino awawa koma tiwasowa koyambiliraku chifukwa anyamata tili nawo oti atha kulowa mmalo mwawo koma sangafike pa iwowa koma nthawi ikapita ndi kuwagayira nzeru afikapo." Anatero Bunya.
Iye wati akufunitsitsa kuti mchigawo chachiwirichi azitolera mapointsi ochuluka kwambiri kuti athere pabwino mu ligiyi.
Timuyi ili pa nambala yachikhumi pomwe ili ndi mapointsi okwana 19 pa masewero 15 omwe yasewera mu ligi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores