NKHANI
Bungwe la Football Association of Malawi lalowa mu mgwirizano ndi banki ya NBS yomwe ithandize ligi ya matimu ang'onoang'ono yadziko lonse omwe akachita bwino azilowa mu TNM Supa ligi.
Izi zadziwika lachitatu pomwe mbali ziwirizi zakumana kuti atsimikize za nkhaniyi komanso kupereka ndalama zomwe zinapezeka mu NBS Charity Shield mu April pomwe FCB Nyasa Big Bullets inagonjetsa Silver Strikers.
Ligiyi iyambe mu chaka cha 2025 ndipo matimu amu ligi yakumpoto, chigawo chapakati komanso kummwera azidzakumana ngati momwe amakumanirana matimu amu Supa ligi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores