"ANYAMATA ASEWERA BWINO ZANGOVUTA" - MWASE
Mphunzitsi watimu ya Mighty Mukuru Wanderers, Meke Mwase, wati osewera atimu yake anasewera bwino kwambiri zinangovuta kuti sanakwanitse kupeza zigoli.
Iye amayankhula atatha masewero omwe afanana mphamvu 0-0 ndi timu ya MAFCO pa bwalo la Chitowe ndipo wati timu yake ilibwino kaseweredwe anangovutika kugoletsa koma wayamikira osewera ake posewera bwino.
"Anali masewero ovuta pang'ono poti nyengo yake ndi yotentha kwambiri koma osewera asewera bwino kwambiri mwina zangotivuta ndi zigoli koma tiwayamikire kuti asewera bwino." Anatero Mwase.
Masewero otsatira a timuyi ndi kukumana ndi FCB Nyasa Big Bullets mu chikho cha FDH Bank ndipo Mwase wati akonzekera bwino kuti adzachite bwino.
Timuyi ili pa nambala yachiwiri mu ligi pomwe ali ndi mapointsi okwana 25 pa masewero 14 omwe yasewera mu ligi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores