"ANYAMATA ASEWERA MMENE NDIKUFUNIRA" - NYAMBOSE
Mphunzitsi watimu ya Chitipa United, Christopher Nyambose, wati ndi wosangalala ndi mmene timu yake yasewera ndi Mzuzu City Hammers ngakhale Iwo agonja mmasewerowa.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 1-0 pa bwalo la Mzuzu ndipo wati timu yake inavutika kuti tipeze chigoli zomwe ndi ntchito yokha yomwe atsala nayo kuti akonze.
"Ndine wokondwa kwambiri poti lero tasewera bwino kwambiri ndipo ndi mmene timu ya Chitipa ndikufuna kuti izisewerera nde zangotivuta ndi zigoli koma angakhale anzathuwa angopezerapo mwayi kuti goloboyi wathu anakanika kugwira mpira koma sanasewere bwino." Anatero Nyambose.
Timu ya Chitipa ikadali ku chigwa cha matimu otuluka mu ligi pomwe ali pa nambala 14 mu ligi ndi mapointsi okwana 9 pa masewero 14.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores