"TIMAYENERA KUTI TICHITE BWINO" - BUNYA
Mphunzitsi watimu ya Premier Bet Dedza Dynamos, Andrew Bunya, wati zinthu sizikuyenda bwino kutimuyi pomwe akufunikira kuti azipeza chipambano cholinga choti akhale pa malo abwino pa ndandanda wa matimu mu ligi.
Iye amayankhula atatha masewero omwe alepherana 2-2 ndi timu ya Kamuzu Barracks pa bwalo la Dedza ndipo wati timu yake ikuyenera kumagoletsa zigoli zambiri zomwe ziwathandizire kuti azitha kupeza chipambano.
"Zinthu sizili bwino timayenera kupambana pa masewerowa koma tachinyitsa zigoli zophweka kwambiri zomwe sizili bwino chifukwa pa ndandanda wa matimu sitili pabwino nde tikuyenera kuti tizipambana mmasewero ngati awawa nde tiyesetsa kukonza kuti zonse ziyende." Anatero Bunya.
Kutsatira kufanana mphamvuku, timuyi ili ndi mapointsi 16 pa nambala 10 mu ligiyi pomwe yasewera masewero okwana 13.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores