"KUPAMBANA KOYAMBA KOYENDA TIKAPANGA NDI HAMMERS" - BUNYA
Mphunzitsi watimu ya Premier Bet Dedza Dynamos, Andrew Bunya, wati timu yake yakonzeka kuti ipeze chipambano chawo choyamba koyenda ndi timu ya Mzuzu City Hammers pomwe akufunitsitsa chipambano chokha akakumana.
Iye amayankhula patsogolo pa masewerowa omwe adzaseweredwe lamulungu pa bwalo la Mzuzu ndipo wati timu yake ikufunitsitsa kuti itolere mapointsi pa masewero atsalawa kuti asunthebe mu ligi.
"Tikukasewera koyenda komwe timaoneka ngati timavutika koma to tikayesetse kuti mwina tikachite bwino pa masewerowa nde anyamata alibwino akudziwa kufunika kwa masewerowa ndipo ndi khumbo lathu kuti tizipambana masewero atsalawa cholinga choti mwina mu ligi tiyimeko pa malo abwino." Anatero Bunya.
Ndipo mphunzitsiyu watsimikiza zakubwera kwa katswiri otseka kumbuyo, Sugzo Mwakasinga, yemwe wachoka posachedwa ku Bangwe All Stars atathetsa mgwirizano wake.
Timuyi ili pa nambala yachisanu ndi chiwiri (7) ndi mapointsi okwana 15 pa m
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores