"TIKUFUNITSITSA TITAKAFIKA MU NDIME YOTSIRIZA" - NTHALA
Mphunzitsi wa otchinga kumbuyo kutimu ya Mighty Mukuru Wanderers, Simplex Nthala, wati timu yawo ichita chilichonse chotheka kuti afike mu ndime yotsiriza ya chikho cha FDH Bank kuti atengeko ukatswiri wa chikhochi koyamba.
Iye amayankhula patsogolo pa masewero awo ndi timu ya Cobbe Barracks pa bwalo la Balaka masana a lolemba ndipo wati ndi khumbo lawo kuti azipambana masewero aliwonse kuti akafike mu ndime yotsiriza.
"Takonzekera bwino kwambiri masewerowa kuti tikachite bwino ndipo osewera akudziwa kufunika kopambana masewerowa nde tikayesetsa kuti tikachite bwino ndikuti tifike mu ndime yotsiriza." Anatero Nthala.
Timu ya Wanderers sinatengeko ukatswiri wa chikhochi chiyambireni mu chaka cha 2021 ndipo chaka chino ati alimbikira kuti achilaweko.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores