"SITINASEWERE BWINO NDIPO EAGLES INALIMBIKIRA" - MPONDA
Mphunzitsi watimu ya Silver Strikers, Peter Mponda, wati timu yake sinasewere bwino mmasewero awo ndi Blue Eagles ndipo nzodabwitsa kuti atuluka mu chikho cha FDH Bank.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 5-3 pa mapenate pa bwalo la Nankhaka masana a lamulungu ndipo wati timu ya Blue Eagles inalimbikira kwambiri zomwe zawathandizira kuti achite bwino mmasewerowa.
"Anali masewero abwino kwambiri koma sitinasewere bwino olo kupambanako tikanangopambanira mwayi koma sitinachite bwino ndipo anzathu a Blue Eagles analimbikira mchifukwa chake apambana." Anatero Mponda.
Iye wati timuyi tsopano iyika chidwi chachikulu ku ligi ya TNM pomwe akuyembekezeka kukumana ndi timu ya Kamuzu Barracks mmasewero otsatira.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores