"MAPOINTSI TSOPANO ATSEGUKA KU BAKA" - MWALWENI
Mphunzitsi watimu ya Baka City, Kondwani Mwalweni, wati tsopano timu yake yapeza poyambira kuti izichita bwino mu ligi pomwe tsopano yapeza chipambano chawo choyamba mu ligi ya TNM.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonjetsa timu ya Bangwe All Stars 2-0 loweruka masana ndipo wati anyamata ake anasewera bwino kwambiri ndiponso anaonetsa mtima wofuna kupambana.
"Tithokoze Mulungu chifukwa chopeza chipambano chimenechi komanso tiyamike anyamata lero agwira Ntchito, anaoneka kuti mtima wopambana ulipo lero nde chipambano choyamba chatipatsa poyambira kuti tipezebe mapointsi ambiri." Anatero Mwalweni.
Timu ya Baka City tsopano yafika pa nambala yachikhumi ndi chisanu (15) ndi mapointsi asanu ndi awiri (7) pa masewero khumi ndi amodzi omwe yasewera.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores