"TIKUNGOYENERA KUPAMBANA BASI" - BUNYA
Mphunzitsi watimu ya Dedza Dynamos, Andrew Bunya, wati kubwerera kwa anyamata angapo kutimu yake omwe anali ovulala kwathandiza kubweretsa mpikisano pakati pa anyamata onse zomwe zithandizire timu yake kuchita bwino.
Iye amayankhula patsogolo pa masewero omwe akumane ndi Karonga United pa bwalo la Dedza Stadium ndipo wati timu yake ikuyenera kupambana kamba koti yafanana mphamvu kambiri mu ligi.
"Sabata yatha tinayesetsa kuti tipambane koma nthawi yothaitha tinakanika nde tafananitsa mphamvu kwambiri tikungofunikira kuti tsopano tipeze chipambano mmasewero athu nde kuona ndi mmene takonzekerera, ndili ndi chikhulupiliro kuti tipambana mmasewero amenewa." Anatero Bunya.
Premier Bet Dedza Dynamos ili pa nambala yachisanu ndi Chinayi (9) mu ligi pomwe ali ndi mapointsi Khumi ndi awiri (12) pa masewero khumi (10).
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores