KAMWENDO, KAFOTEKA, JOMO OSMAN NDI ENA APHUNZIRA CAF B
Osewera akale a Flames, Joseph Kamwendo, Elvis Kafoteka, Robert Ng'ambi, Heston Munthali ndi Jimmy Zakazaka ali ndi mwayi woti posachedwa atha kukhala ndi matimu omwe aziphunzitsa mu TNM Supa ligi kamba koti akaphunzira maphunziro a CAF B.
Bungwe la Football Association of Malawi latsimikiza za nkhaniyi kuti aphunzitsi okwana 25 ndi omwe apite ku maphunzirowa omwe bungweli lichititse mu mwezi wa August pofuna kuchulutsa aphunzitsi ovomerezeka mdziko muno.
Maphunzirowa adzakhala kwa miyezi iwiri kuchokera pa 18 August mpaka pa 18 October chaka chino. Kupatula osewera akalewa, mwini wake wa Ntopwa FC, Isaac Jomo Osman, mwini wake wa Zingwangwa United, Dida Zingwangwa komanso a Davie Mpinga Jr aku Mpira Mmudzi Mwathu ali mu gululi.
Aphunzitsi aakazi atatu, Chisomo Nkhoma wa Chisomo Academy, Linda Kasenda komanso Caren Chawula ali nawonso pa ndandanda umenewu.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores