"ANZATHU ANATIBALALITSA NDI MIPIRA ITALIITALI" - KUMWEMBE
Wachiwiri kwa othandizira mphunzitsi kutimu ya MAFCO, Macdonald Kumwembe, wati kugonja kwawo ndi timu ya Creck Sporting Club ndi kopweteka chifukwa sanayembekezere kuti zikhonza kuyenda choncho.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 1-2 ndi timu ya Creck ndipo iye wati timu yake inabalalika ndi maseweredwe a anzawowo omwe samasunga mpira koma kumenya wautaliutali basi.
"Ndi kugonja kopweteka kwambiri chifukwa sitinaganizire kuti zithers koma poti mpira wochinya zigoli zambiri ndi yemwe amakhala kuti wapambana. Anatisokoneza mmene anabwerera mchigawo chachiwiri chifukwa samapatsirana koma amamenya wautaliutali nde koma tikakonza tikabwerera." Anatero Kumwembe.
Timu ya MAFCO ili pa nambala yachikhumi ndi chitatu (13) pomwe ali ndi mapointsi asanu ndi anayi (9) pa masewero asanu ndi anayinso (9).
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores