"TIKANATHA KUGOLETSANSO ZINA ZAMBIRI" - BUNYA
Mphunzitsi watimu ya Dedza Dynamos, Andrew Bunya, wati timu yake ikhazikika pa chidwi chogwiritsa ntchito kwambiri mipata yomwe anayipeza mchifukwa chake akwanitsa kupambana masewero awo oyamba mu 2024.
Iye amayankhula atatha masewero omwe apambana 3-0 ndi timu ya MAFCO pa zigoli zomwe zinafika mchigawo choyamba ndipo wati timu yake ikanathanso kupeza zochuluka kuposa zimenezi.
"Anali masewero ovuta ndipo timadziwa kuti avuta chifukwa anzathunso amafuna kupambana koma tinangosamala kuti tipeze mipata yochuluka ndipo tiyigwiritse ntchito, ndithokoze anyamata anakwanitsa kutero koma tikanathanso kupeza mipata yambiri." Anatero Bunya.
Iye wati chipambano chimenechi chipereke mphamvu kutimu poti tsopano anyamuka mu ulendo wawo wofuna kuchita bwino mu 2024.
Timuyi ili ndi mapointsi asanu ndi imodzi (6) pomwe yagonja kamodzi, kufanana mphamvu katatu ndi kupambana kamodzinso ndipo ali pa nambala Khumi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores