"SITINALI BWINO BASI" - MZUNGA
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya MAFCO, Jimmy Mzunga, wati timu yake yakanika kuchita bwino mmasewero awo kamba koti sanali bwino mmasewerowa.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 3-0 ndi Dedza Dynamos ndipo anagoletsetsa mu mphindi 40 za mchigawo choyamba koma iye wati pompano sizintha.
"Tagonja zoonadi, sizinali bwino sitinali bwino kuchoka pachiyambi mpake tagonja. Tikuona mavutowa ndipo tikonza." Watero Mzunga.
MAFCO ndi imodzi mwa matimu omwe sanapezebe chipambano mu ligi ya 2024 pomwe agonja katatu ndi kufanana mphamvu kawiri kuti akhale ndi mapointsi awiri pa masewero asanu ndipo ali pa nambala 15.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores