PREMIER BET KU SUPER LEAGUE
Kampani ya Premier Bet yapereka ndalama zokwana K260 million zomwe zigwire ntchito kupereka mphoto zosiyanasiyana mu ligi ya 2024.
Mwa zina:
•K160 million iperekedwa Kwa matimu 16 omwe agawane K10 million.
•K20 million ipita pa uniform yomwe ikhale ndi dzina la kampaniyi.
•K1.8 million ipita ku gawo la osewera ochita bwino pa mwezi yemwe azitenga K200,000.
•K1.8 million ina ipita Kwa aphunzitsi abwino pa mwezi pomwe aliyense azitenga K200,000.
•K9.9 million ikupita Kwa timu yabwino pamwezi pomwe iliyonse izitenga K1.1 million.
•K900,000 ipita ku mbali ya atolankhani pomwe K100,000 pa mwezi izipita Kwa mtolankhani mbambande pa mwezi ku zamasewero.
Bungwe la SULOM lalengeza za izi kudzera pa tsamba lawo la mchezo.
Reported by Hastings Wadza Kasonga Jr
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores