"CHITIPA IWONJEZANO MOTO" - KAFOTEKA
Wachiwiri wa mphunzitsi wamkulu ku Chitipa United, Elvis Kafoteka, wati ndikhumbo lake kuti anthu onse kutimuyi agwirire ntchito limodzi ndi cholinga choti adutse pomwe anafikira chaka chatha.
Kafoteka wayankhula patsogolo pa ligi ya chaka chino ndipo walonjeza kunena kuti ayesetsa kuthandiza timuyi kuti ifikire ku mtunda kwa matimu atatu oyambilira mu ligi.
"Ndingopempha kuti tonse tigwirane manja kuti zikatero tikhonza kudutsa pomwe tinafika chaka chatha ndipo tikhonza kukakhazikika kumtunda kwenikweni kwa ligiyi. Chaka chino kuli moto wochuluka ku Chitipa." Anatero Kafoteka.
Iye agwira ndi a McNerbert Kadzuwa ngati mphunzitsi wamkulu pomwe a Gift Mkamanga ndi wachiwiri wake. Timuyi Inathera pa nambala yachinayi mu ligi ya chaka chatha.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores