"AYI! AYI! SITINAGULITSE MASEWERO" - MKANDAWIRE
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Red Lions, Malumbo Mkandawire, wati timu yake inavutika kwambiri kamba koti Moyale inawapanikiza kwambiri makamaka mchigawo chachiwiri.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 7-0 pa bwalo la Mzuzu ndipo wati timu yake sinagulitseko masewerowa koma kungoti zawavuta basi.
"Masewero sanali abwino poti sitinasewere bwino komanso kuti Moyale inatipanikiza kwambiri nde zinapangitsa kuti atichinye zigoli zambiri. Ayi ayi sikuti chifukwa choti tonse ndi asilikali ayi koma anzathuwa anatipanikiza kwambiri nde tikaphwasulanso timuyi ndi kukonzanso." Anatero Mkandawire.
Red Lions imapita mmasewerowa ikudziwika kale kuti yatuluka ndipo mchigawo choyamba imatsalira 1-0 ndipo zisanu ndi chimodzi zinazo zabwera mchigawo chachiwiri. Timuyi yamaliza ndi mapointsi 29 pa masewero 30.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores