KODI NKHANI YA ALFRED MANYOZO ILIPATI?
Papitano miyezi yoposera inayi timu ya Mighty Mukuru Wanderers itayimitsa katswiri wawo, Alfred Manyozo Jr, kutsatira ndi kukwiya kwa masapota awo kuti katswiriyu asiye kusewera.
Owinna ikhonza kutsimikiza kuti Manyozo akuyenera kumawerengera za ligi ya chaka Chatha pomwe chaka chino nkhani yake ikuoneka kuti sikhudzidwa kutimuyi.
Akuluakulu atimuyi anati amuitana Manyozo akafufuza malipoti oti akumayankhula mosakhala bwino kwa osewera anzake komanso kuti amapanga ziganizo zochuluka kusiyana ndi aphunzitsi komatu mpaka pano palibe chachitika.
Mmbuyomu Owinna inalengeza kuti nkhani ya Manyozo sikhudzidwa kamba koti timuyi inayamba kuchita bwino atachoka ndipo mpaka pano palibe yemwe wayitosako.
Katswiriyu ndi mmodzi mwa osewera okhalitsa kutimuyi ndipo wapambana zikho zisiyanasiyana kuphatikiza ligi ya TNM mu chaka cha 2017.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr
Ikhale ligi ya chaka cha mawa
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores