KARONGA YATOLA KAJAWA
Timu ya Karonga United yalemba ntchito mphunzitsi wakale kutimu ya Mighty Wakawaka Tigers, Trevor Kajawa, kuti atsogolere timuyi.
Karonga yatenga Kajawa kutsatira chilango chimene anapatsidwa ndi bungwe la Football Association of Malawi kamba kogwiritsa ntchito mphunzitsi wopanda mapepala a CAF B, Luka Milanzie.
Timuyinso inauzidwa kuti Milanzie asaonekenso akutsogolera timuyi zomwe zimaonetsa kuti akanamasewera masewero awo wopanda mphunzitsi.
Kajawa waphunzitsapo Tigers Tigers kangapo mmbuyomu ndipo ali ndi sukulu yake ya mpira yomwe imatchedwa kuti Kangaroo Academy.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores