CHOTSATIRA NDI CHIYANI KWA MANYOZO JR
Katswiri wa Mighty Mukuru Wanderers, Alfred Manyozo Jr, sabwereranso pa bwalo lazamasewero posachedwa pomwe zamveka kuti timuyi sikuikhudzako nkhaniyi.
Mmodzi mwa anthu amkati mwa timuyi awuza Owinna kuti nkhani ya Manyozo sikufukulidwa kamba koti kuchoka kwake timu ikuchita bwino.
"Nkhani imene ija isiyeni chifukwa palibe wamkulu yemwe akufuna kuikamba chifukwa timu yayamba kuwina iye atangochoka." Mkuluyu anafotokoza.
Papita tsopano mwezi ndi masabata awiri chimuimitsireni katswiriyu pomwe masapota ankafuna kumumenya kamba koti akuononga timu ndiponso ndi malipoti oti osewera ambiri akumudandaula.
Timuyi tsopano yakhulupilira Stanley Sanudi kuti azisewera pa malo a Manyozo pomwe tsopano ali pa nambala yachinayi mu ligi ndi mapointsi 29 pa masewero 16.
Walk well
Sante nankhukwa maida@
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores