RAPSON AKUFUNA KUSIYANA NDI BLUE EAGLES
Katswiri wakale watimu ya Mighty Mukuru Wanderers komanso Hangover FC, Richard Rapson, walembera kalata timu ya Blue Eagles kupempha kuti athetse mgwirizano wake ndi timuyi.
Mu kalata yomwe walemba katswiriyu ndipo yadutsira ku Football Association of Malawi komanso Super League of Malawi, yati katswiriyu wakhala asakulipilidwa kuchokera mu mwezi wa January kamba ka zifukwa zomwe Blue Eagles imadziwa yokha.
Malipoti akuti osewerayu anauzidwa kuti amvetsedwa kuti ali ku Mighty Mukuru Wanderers ndipo tsopano sangamulipire ndalama zilizonse.
Zikatheka, katswiriyu akhonza kulowera ku imodzi mwa matimu pakati pa Premier Bet Dedza Dynamos komanso Civil Service United kumathero a sabata ya mawayi.
Zoona zake tikudandaula kwainu amumba ndalamayi itafikadi pa k50000 tingamapikisane kwambili komaso ena angabweleso atsopano ndiwomwe anasiyaso.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores