Oimbira masewero a mpira wamiyendo kuno ku Malawi amalandira ndalama zochepa kuyelekeza ndi anzawo m'maiko ena.
Malingana ndi bungwe loyang'anira oimbira masewero mdziko muno, lifali aliyense amalandira K26, 000 akaimbira masewero.
Mlembi wa bungweli, Chris Kalichero wati izi ndi ndalama zochepa kwambiri kuyelekeza ndi maiko ena.
Mwachitsanzo, oimbira masewero aku South Africa amalandira aliyense K335, 500 akaimbira masewero.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores