"TIKADAKONDWA CHIKADAKHALA KUTI CHIGAMULO CHATSIKABE" - MICKEUS
Woyimira milandu bungwe la Football Association of Malawi pa mlandu wokhudza mphunzitsi wakale wa Flames, Patrick Mabedi, wati chigamulo chomwe bwalo la milandu loona za malamulo a ntchito lapereka kuti FAM ipatse Mabedi K53.6 million ndi chabwino.
Iye amayankhula pofotokozapo za momwe mlanduwu wayendera kufikira kumapeto komwe bwaloli lapereka chigamulochi.
Iye wati poyamba, a Mabedi anapempha kuti alipilidwe K916 million ngati chipepeso pa kuchotsedwa ntchito kwawo mosatsata malamulo koma iwo anapempha kuti chipepesochi chitsike.
"Titapempha bwalo linaunikira ndipo lanena kuti tipereke pafupifupi K54 million ndipo ndikuona ngati chigamulochi chayendabe bwino koma ndikadakonda akadatsitsako pang'ono," anatero Mickeus.
A Mabedi anakamang'ala ku bwalo la milandu kutsatira kuchotsedwa kwawo kwa ntchito atagwira miyezi khumi ndi umodzi pa mgwirizano wa zaka ziwiri womwe anasaina.
FAM inachotsa a Mabedi posakhutira ndi z
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores