EKHAYA IKUPITILIRA KUVUTIKA MU LIGI
Zinthu sizikuyendabe kutimu ya Ekhaya FC mu chaka chawo chachiwiri mu ligi yaikulu pomwe yagonja kachiwiri mu ligimu ndi timu ya Civil Service United 1-0 pa bwalo la Civo loweruka masana.
Timuyi yayamba udyo mu ligi angakhale kuti yaonjezera osewera ena apamwamba kuchokera ku matimu osiyanasiyana pomwe inafananitsa mphamvu kamodzi ndi kugonja kamodzi asanalowe mu masewerowa.
Civil inamwetsa chigoli chake mu mphindi 10 za masewerowa kudzera mwa John Dambuleni kuti achite bwino mu masewerowa.
Wachiwiri kwa mphunzitsi wa timuyi, Moses Chavula, wati kugoletsetsa chigoli mofulumira ndi kumene kunawabalalitsa mu masewerowa.
"Kwinako timasewerano mwa phuma kuti tibwenze koma sizinatheke. Tili ndi timu yabwino yomwe tikangopambana kamodzi ndekuti osewera akhala kuti alimba mtima tsopano," iye anatero.
Chavula anatinso timuyi kwachuluka osewera atsopano omwe sanakhazikike ndipo zitengapo kanthawi kuti atero.
Ekhaya yatsika kufika pa nambala 14 kutsatir
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores