"KWANGA NDACHITA KWATSALA KWA OSEWERA" - CHATAMA
Mphunzitsi watimu ya Ekhaya FC, Enos Chatama, wati osewera a timuyi akuyenera kutenga udindo tsopano womapanga zimene aphunzitsi akuwauza kamba koti zonse akumauzidwa koma akumakanika kugwiritsa ntchito.
Iye amayankhula atatha masewero omwe alepherana 1-1 ndi timu ya Red Lions ndipo wati timu yake yaphonya mipata yochuluka yomwe ikanakwanitsa kuwapatsa chipambano.
"Sikuti sanagwirane ayi chifukwa ngati akukwanitsa kupatsirana kupita kutsogolo ndi kukaphonya poti palibepo goloboyi ndekuti timu ilibwino koma udindo wa zinazi ndi womwe akufunikira ndekuti zitha kuthandiza," anatero Chatama.
Iye wati anthu asadere nkhawa kamba koti atha kuyamba movutira koma nkudzamaliza bwino popereka zitsanzo za Manchester City ndi Liverpool aku Mangalande.
Ekhaya ili pa nambala 12 mu ligi pomwe ili ndi point imodzi pa masewero awiri omwe yasewera.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores