Creck yaitanidwa ku Mozambique
Matimu omwe akukachita zokonzekera zawo mu dziko la Mozambique akwana tsopano atatu pomwe timu ya Creck Sporting Club yaitanidwa mdziko la Mozambique kukasewera nawo mu mpikisano wokonzekera mu ligi ya chaka cha 2025.
Timuyi yatsimikiza za nkhaniyi lolemba madzulo kudzera pa tsamba lawo la Facebook kuti timu ya Ferroviario de Lichinga ndi yomwe yawaitana mu mpikisano wa masiku awiri.
Timuyi yati ndi yokondwa pori izi zilimbikitsa ubale wao ndi matimu amdzikomo zomwe ndi zinthu za mtengo wapatali.
Mpikisanowu udzayamba loweruka pa 15 March 2025 ndi kutha mawa lakelo pa 16 March.
Matimu a Mighty Wanderers komanso Civil service United nawo ayitanidwanso ndi timu ya UD Songo ku mpikisano wa matimu anayi mmasiku omwewanso.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores