Wanderers ikalambula bwalo ku Mozambique
Mayere a mpikisano wokonzekera ligi ya chaka cha 2025 achitika pomwe Mighty Wanderers idzayambilire kusewera ndi timu ya Chingale de Tete pasanabwere masewero a UD Songo ndi Civil Service United.
Izi zadziwika pomwe timu ya UD Songo yalengeza kudzera pa tsamba lawo la Facebook lachiwiri.
Masewero a Wanderers ndi Chingale adzayamba kota tu 2 pomwe a Songo ndi Civil adzayamba kota to 4.
Opambana mmasewerowo oterewa adzafika mu ndime yotsiriza ya mpikisanowu yomwe idzaseweredwe lamulungu masana.
Timu ya Wanderers inapitakonso ku Mozambique komwe inaseweranso masewero apaubale mu 2017 yomwe anakwanitsa kutenganso ukatswiri wa ligi.
Matimu onse aku Mozambique awa kumasewerako a Malawi pomwe ku Songo kuli Yamikani Chester ndi Richard Mbulu pomwe ku Chingale yomwe yangolowa kumene mu ligi yaikulu kuli Clement Chipanda yemwe waseweraponso Dedza Dynamos.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores