MWAUNGULU AKUCHITA BWINO KU DRC
Katswiri wosewera pakati mu timu ya Flames, Patrick Mwaungulu, anasankhidwa kukhala osewera yemwe wasewera mwapamwamba pomwe timu yake ya CS Don Bosco inagonjetsa Groupe Bazano 2-0 mu ligi yaikulu yaku DRC lolemba.
Iye anagoletsako chigoli chimodzi chomwe chathandiza Timuyi kufika pa nambala yachisanu ndi chimodzi mu gulu lomwe muli matimu khumi ndi awiri pomwe Ali ndi mapointsi 23 pa masewero 18.
Katswiriyu ali kutimuyi pangongole kuchokera kutimu ya TP Mazembe yomwe inamugula kuchoka ku FCB Nyasa Big Bullets pamodzi ndi Lanjesi Nkhoma.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores