Chisankho chakumpoto chaimitsidwa
Chisankho chomwe chimachitika ku bungwe loyendetsa mpira mchigawo chakumpoto chasunthidwa tsiku kamba koti opambana pa mpando wa wapampando ku bungweli samapezeka.
Wapampando yemwe anali ku bungweli, Chauka Mwasinga, amapikisana ndi mlembi wamkulu, Masiya Nyasulu pa mpandowu koma kawiri konse iwo apeza mavoti 13-13.
Malingana ndi uthenga womwe walembedwa pa tsamba la mchezo la Facebook la bungweli, chisankhochi sichipitilira ndipo masiku atsopano alengezedwa mtsogolomu.
Ilo lati bungwe la Football Association of Malawi ndi limene lipereke chitsogozo cha mmene zisankhozi zichitikire kutsogoloku.
Ngakhale zili chomwechi, maudindo omwe amagwira kwa zaka zinayi zapitazi kufikira mu tsiku la lero akhalabe asali mmanja mwa adindo akalewa.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores