Pasuwa azifika ku matimu onse
Mtsogoleri wa bungwe la Football Association of Malawi, Fleetwood Haiya, wati Kalisto Pasuwa athandizira kukhazikitsa kamenyedwe (philosophy) ya dziko lino pomwe adzifikanso mu matimu achisodzera ndi ya amayinso.
Haiya amayankhula pa mwambo woonetsa mphunzitsiyu kwa anthu atasaina mgwirizano wa zaka ziwiri ndi bungweli.
Iye wati Pasuwa athandizira kupititsa patsogolo mpira wa mdziko muno ndipo ali ndi mphamvu zochuluka zomwe akhale nazo pa ntchito yake.
"Sikuti akhale ku Flames kokha komanso azifika kwa achisodzera paja chaka chino tikukhazikitsa maseweredwe athu nde azionetsetsa ngati zikutheka kumatimuwa angakhalenso ku Scorchers azifika." Anatero Haiya.
Pasuwa akhale mphunzitsi wokhazikika wa timu ya dziko lino mpaka mu 2027 ndipo posachedwapa atsogolera Flames mu CHAN komanso mu masewero opita ku World Cup.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores