FAM yalonjeza kuthandiza Pasuwa
Bungwe la Football Association of Malawi lalonjeza kuti lipereka thandizo lokwanira kwa mphunzitsi watsopano kutimu ya Flames, Kuti athandize kupititsa patsogolo masewero a mpira.
Mtsogoleri wa bungweli, Fleetwood Haiya, amayankhula pomwe mphunzitsiyu amaonetsedwa kudziko lonse atapatsidwa mgwirizano wa zaka ziwiri.
Iye wati tsopano Pasuwa wapatsidwano mphamvu poti si ogwiriziranso ndipo akuyembekezera zabwino zokhazokha kwa mphunzitsiyu.
"Tsopano ndi nkhani yabwino kuti Pasuwa ali ndi mphamvu. Tiyesetsa kumupatsa sapoti yonse kuti iyeyu achite bwino ndi kutengera mpira wathu patsogolo." Anatero Haiya.
Pasuwa anali mphunzitsi wogwirizira watimuyi ndipo pamasewero omwe anaphunzitsa, Malawi inalepherana 0-0 ndi Burundi komanso kugonjetsa Burkina Faso 3-0.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores