Haiya: Sitinaphonyeko ndondomeko
Mtsogoleri wa bungwe la Football Association of Malawi, Fleetwood Haiya, wati bungweli linatsata ndondomeko zonse zoyenera kuti alembe Kalisto Pasuwa kukhala mphunzitsi wa Flames.
Iye amayankhula pa mwambo oonetsa mphunzitsiyu kwa anthu a mdziko muno atasaina mgwirizano wa zaka ziwiri ndi bungweli.
Motsutsana ndi bungwe la Malawi National Council of Sports lomwe linadzudzula FAM ati posatsata ndondomeko polemba mphunzitsi, iye anati palibe chinali cholakwika.
"Tinapeza bungwe la aphunzitsi omwe anavomera Pasuwa kenako tinapita ku sub technical committee inavomeranso, kenako komiti yaikulu tinavomeranso nde panalibe cholakwika ndithu." Anatero Haiya.
Pasuwa yemwe kwawo ndiku Zimbabwe wakhala mphunzitsi wogwirizira watimuyi asanatengeretu ntchitoyi ndipo akhale kufikira 2027.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores