Mtsogoleri wa bungwe la Football Association of Malawi, Fleetwood Haiya, akhala akuyankhulana ndi anthu mdziko muno pofuna kumva maganizo awo pa momwe mpira mdziko muno ungatukukire.
A Haiya analengeza za dongosololi mwezi watha ndipo zatsimikizika kuti achita mwambowu lero pa 6 February 2025 nthawi ya 8 koloko.
Iwo akhale ali pa tsamba lawo la Facebook ndipo ndemanga za anthu omwe akuwatsatira ndi zomwe zitsatilidwe.
Anthu okwana khumi akhale akupeza ma T-shirt kamba kotenga nawo mbali pa mwambowu.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores