HAIYA WATI OYIMBIRA ONSE AZIPATSIDWA ZITUPA ZA MDZIKO MUNO
Mtsogoleri wa bungwe la Football Association of Malawi, Fleetwood Haiya, wati ali ndi ganizo loti oyimbira a mdziko muno azikhalanso ndi chitupa cha mulingo wapa dziko ndipo yemwe azipalamula azilandidwa.
Iye amayankhula pa mwambo umene amapereka zitupa za pansi pa bungwe la FIFA kwa oyimbira mpira wamiyendo khumi ndi awiri (12) komanso a masewero apagombe awiri.
Iye wati FAM ikhale ikubweretsa chitupa chapadziko ngati momwe chilili cha FIFA kuti mwina oyimbira azilimbikira komanso izitha kuchotsedwa kwa iwo ngati apalamula.
"Chitupa chimenechi chizipereka chilimbikitso kwa oyimbirawa komanso kuwapangitsa kugwira ntchito moyenerera ndi kubweretsa chikhumbokhumbo chopeza chitupachi zikatero mpira upita patsogolo." Iye anafotokoza.
Haiya anatinso yemwe adzapezeke olakwa pa milandu ina ndiye kuti azidzalandidwa chitupachi.
Oyimbira osankhika okha ndi bungwe la FIFA ndi omwe amakhala ndi chitupa pomwe ena omwe sanasankhidwe sapatsidwa angakhale kuti amayimbiranso mu ligi yaikulu.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores