FOMO: Tikufuna kubwerera mu Supa ligi pompano
Timu ya FOMO FC yati ikufunitsitsa kusunga osewera omwe amagwiritsa mu Supa ligi cholinga choti awathandize kubwerera mu ligi posachedwapa poti padakali pano ali ndi luso kale losewera mu ligi yaikuluyi.
Mlembi wamkulu watimuyi, Jimmy Maloya, amayankhula izi pomwe amatsimikiza kuti asewere nawo mu ligi yaing'ono yadziko lonse yomwe ikuyambika mu chaka chino.
Iye wati iwo ndi khumbo lawo lobwereranso mu ligiyi ndipo nkhani yake ndi yosewera mu ligi yaing'onoyi.
"Tikukhulupilira kuti tikhale ndi osewera omwe timagwiritsa mu Supa ligi poti tsopano ali ndi ukadaulo wokwana ndipo ziphweka kubwereranso mu ligi." Anatero Maloya.
Pa nkhani ya mphunzitsi, iye wati timu ikabwerera ku tchuthi, akhale akulongosola koma malingana ndi malipoti, Elvis Kafoteka saonekako kutimuyi ndi Jimmy Zakazaka atha kutenga timuyi.
FOMO inatuluka mu ligi ya TNM itangosewera kwa chaka chimodzi pomwe inathera pa nambala 14.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores