BULLETS YASIYANA NDI OSEWERA 9
Timu ya FCB Nyasa Big Bullets yakhala yoyamba kuchotsa osewera mu ligi ya chaka cha 2025 pomwe yalengeza mayina asanu ndi anayi omwe akhale akusuntha kutimuyi.
Timuyi yatsimikiza za mayinawa kudzera pa tsamba lawo la mchezo masana a lachisanu pomwe osewerawa sali mu dongosolo la aphunzitsi ndipo ena achoka atakambirana ndiponso ena migwirizano yatha. Osewerawa ndi:
Colin Mujuru Felix Demakude Kesten Simbi Matthews Masamba Mphatso Magaleta Precious Phiri Thomson Magombo Ronald Chitiyo Kenneth Pasuwa
Ndipo timuyi yati yapereka migworizano yoonjezera kwa osewera monga Gomegzani Chirwa, Stanley Biliati komanso Nickson Nyasulu ndipo zili ndi iwo kuti asayine.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores