Bungwe loyendetsa masewero a mpira wa miyendo la Football Association of Malawi tsopano latulutsa chigamulo pa za katswiri wa timu ya FCB Nyasa Big Bullets Hassan Kajoke pa mulandu wake.
FAM yagamula motere;
Osewerayu, Hassan Kajoke, abweze MK3.9 million ku team ya Silver Strikers pasanathe masiku asanu chitulutsireni chigamulochi ndipo ngati satero, adzaimitsidwa kusewera mpira kuno ku Malawi ndikunja.
Ngati satero, adzaimitsidwa kusewera mpira kuno ku Malawi komanso kunja ndipo ndalamayi idzabwezedwa ndi chiongola dzanja chovomerezeka pa msika osintha ndalama akadutsa masiku asanuwa.
Timu ya Silver Strikers ipereke account kwa Hassan Kajoke yoti ayikeko ndalamazi ndipo timu imeneyi idziwitsenso nthambi yowona za osewera ku bungwe la FAM ngati ndalamayo yaperekedwa kapena ayi.
Zonse zomwe idapempha Silver Strikers (kupatulako zokhudza ndalama zomwe Hassan Kajoke adatenga) zakanidwa, pajatu timu'yi idapempha kuti osewerayu amuimitse pamodzi ndi omuyimilira wake.
[DELETED]
Silver Strikers ayipeza olakwa kamba kosaina osewera oti siwawo, kotera Silver ayilamula kuti ilipire MK900 000 pasanathe masiku asanu chitulutsireni chigamulochi.
Ngati izi sizichitika, timu'yi ipatsidwa chilango chosagula ndikulembetsa osewera kwa zaka ziwiri.
Hassan Kajoke wauzidwanso kuti alipire MK 200 000 ku FAM ngati chilango pa zomwe anachita ndipo ngati satero, adzaimitsidwa kusewera mpira mpaka atalipira mlandu wakewu.
Oyimira osewerayu, Ken Mvula walamulidwa kuti alipire MK 500 000 pasanathe masiku asanu kamba kopusitsa munthu.
Ngati satero iyeyu sadzaloledwa kukhalanso mkhala pakati wa osewerayu kapena osewera aliyense muno M'malawi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores