Bungwe loyendetsa masewero a mpira wa miyendo la Football Association of Malawi tsopano latulutsa chigamulo pa za katswiri wa timu ya FCB Nyasa Big Bullets Hassan Kajoke pa mulandu wake.
FAM yagamula motere;
Osewerayu, Hassan Kajoke, abweze MK3.9 million ku team ya Silver Strikers pasanathe masiku asanu chitulutsireni chigamulochi ndipo ngati satero, adzaimitsidwa kusewera mpira kuno ku Malawi ndikunja.
Ngati satero, adzaimitsidwa kusewera mpira kuno ku Malawi komanso kunja ndipo ndalamayi idzabwezedwa ndi chiongola dzanja chovomerezeka pa msika osintha ndalama akadutsa masiku asanuwa.
Timu ya Silver Strikers ipereke account kwa Hassan Kajoke yoti ayikeko ndalamazi ndipo timu imeneyi idziwitsenso nthambi yowona za osewera ku bungwe la FAM ngati ndalamayo yaperekedwa kapena ayi.
Zonse zomwe idapempha Silver Strikers (kupatulako zokhudza ndalama zomwe Hassan Kajoke adatenga) zakanidwa, pajatu timu'yi idapempha kuti osewerayu amuimitse pamodzi ndi omuyimilira wake.
[DELETED]
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores