Mphunzitsi wamkulu wa Silver Strikers Pieter De Jongh wayitanisidwa mkachipinda komata katimuyi kamba kosowa khalidwe.
A Jongh pamasewero anayi omwe Silver yasewera alandira ma yellow card awiri ndi red card imodzi zomwe zawakhuza akuluakulu a Silver kuti amufunse kuti chikuvuta ndichani.
Mbali ina, bungwe la oyimbira masewero ampira wamiyendo a dziko lino la National Referees Association (NRFA) lapempha Super league of Malawi (Sulom) kuti lipereke chilango kwa Pieter De Jongh.
A Jongh ati akusowa khalidwe pamene akumalimbana ndi oyimbira posagwilizana ndiziganizo zawo.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores