Creck ndi Bullets akumana pa Nankhaka
Bungwe la Football Association of Malawi lalengeza kuti masewero achibwereza amu chikho cha Airtel Top 8 pakati pa Creck Sporting Club komanso FCB Nyasa Big Bullets aseweredwe lowerukali pa bwalo la Nankhaka mu mzinda wa Lilongwe.
Bungweli latsimikiza za masiku atsopano a masewero a chikhochi pomwe kumathero a sabatayi, matimu awiri azigulire malo mu ndime ya matimu anayi a mchikhochi.
Creck igwiritse ntchito pa Nankhaka kamba koti bwalo lomwe analembetsa la Aubrey Dimba silinalandire chilolezo chochititsa masewero ama ligi akulu akulu. Masewero onse ayende motere:
Loweruka, 26 April 2025
-Creck Sporting Club (0) vs (0) FCB Nyasa Big Bullets @ Nankhaka Stadium
Lamulungu, 27 April 2025
-Karonga United (0) vs (1) Mighty Wanderers @ Karonga Stadium
Loweruka, 17 May 2025
-Moyale Barracks (0) vs (1) Silver Strikers @ Silver Stadium
Lamulungu, 18 May 2025
-Civil Service United (0) vs (0) Mzuzu City Hammers @ TBC
Masewero amu ndime ya matimu anayi