"KUPAMBANA KUTITHANDIZA KUTI TIKHAZIKIKE KWAMBIRI" - MPONDA
Mphunzitsi watimu ya Masters Football Club, Peter Mponda, wati timu yake ikukumana ndi timu yovuta kwambiri ikakhala pa kwawo koma kupambana kuwathandizire kukhazikika mu ligi.
Iye amayankhula patsogolo pa masewero awo ndi Karonga United ku Karonga lamulungu ndipo wati akukhulupilira kuti akonzekera bwino.
Mponda wati sangawerengere kuti anapambana mu masewero okonzekera ligi poti matimu ambiri samayang'ana zopambana mu masewero oterewa.
"Ifeyo takonzekera bwino ndipo ndili ndi chikhulupiliro kuti tikachita bwino koma Karonga ndi timu yovuta yomwe ili ndi anyamata ovuta komabe tikayesetsa chifukwa tikapambana tikhala ndi chikhulupiliro kuti tizichita bwino," anatero Mponda.
Iye wati timuyi sikhala ndi Chisomo Mpachika kwa masabata awiri yemwe ndi wovulala.
Masters ili pa nambala yachitatu mu ligi pomwe ili ndi mapoints atatu pa masewero amodzI.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores