CIVIL SINAKHUTIRE NDI OYIMBIRA
Mphunzitsi watimu ya Civil Service United, Abbas Makawa, wati wakhumudwa ndi momwe ligi yayambira pomwe wati timu yake imayenera kupambana koma kukondera kwa oyimbira kwawalepheretsa.
Iye amayankhula atatha masewero omwe alepherana 2-2 ndi timu ya FCB Nyasa Big Bullets pa bwalo la Civil mokwiya kwambiri.
Timuyi inatsutsana ndi chiganizo cha oyimbira pa chigoli chachiwiri cha Bullets pomwe amakhulupilira kuti goloboyi wawo anagundidwa koma oyimbira anakana.
Iye anati, "Mwaona kale momwe tasewerera, pakadakhala kuti panali chilungamo bwenzi titapambana koma ndakhumudwa kwambiri kuti tikuyamba ndi kukondera motere."
Mmasewerowa, Bullets inatsogola kawiri ndi zigoli za Clever Kalambo komanso George Chaomba koma John Dambuleni ndi Khumbo Mhone amabwenza.
Civil tsopano ili pa nambala yachiwiri ndi point imodzi pa masewero amodzi mu ligiyi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores