"ANYAMATA SANAGWIRANE BWINOBWINO" - MTETEMERA
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Mighty Wanderers, MacDonald Nginde Mtetemera, wati timu yake yagonja ndi Goshen City Dedza Dynamos kamba koti anyamata ake sanagwirane bwinobwino.
Iye anayankhula kutsatira kugonja pa mapenate 4-2 kuti akanike kufika mu ndime yotsiriza ya chikho cha Sapitwa Big Four pa bwalo la Mulanje Park loweruka.
Iye wati ndi wokhutira ndi mmene osewera asewerera ndipo ubwino ndi wakuti agonja mmapenate.
"Anyamata sanagwirane zomwe zaoneka kuti zativuta kuti tipeze zigoli koma taonaona movutamo ndipo tiyesetsa kukonza kuti tichite bwino," iye anatero.
Zateremu, Manoma akumana ndi Red Lions polimbirana pa nambala yachitatu lamulungu ndipo Nginde wati adzapambana mmasewerowa.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores