NKHANI
Timu ya Mighty Wanderers yalengeza kuti goloboyi wa timu ya Chitipa United, Jacob Anyandwire, wafika kutimuyi komwe wasaina mgwirizano wa zaka zitatu ndi Manoma.
Goloboyiyu wachoka ku timu ya Chitipa komwe anakwanitsa osagoletsetsa mu masewero 12 mu ligi ya chaka cha 2025.
Iye waseweraponso mu ligi yaku Tanzania ndi timu ya Malindi Sports Club asanapite ku Chitipaku.
Iye wakhala wachisanu kutengedwa ndi timuyi pambuyo pa Lameck Mithi, Dalitso Nahipa, Alex Kambirinya ndi Peter Ng'ambi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores