CAF YASINTHA MASIKU A WAFCON
Bungwe loyendetsa mpira mu Africa la Confederation of African Football lasintha masiku a mpikisano wa Womens African Cup of Nations kufikira mu mwezi wa July.
Bungweli linakonza kuti mpikisanowu udzayamba pa 17 March mpakana pa 3 April koma zambiri zakhala zikukambidwa zokhudza kusuntha masikuwa.
Matimu omwe amayenera kusewera ku mpikisanowu kuphatikiza dziko la Malawi anali pa kalikiliki kukonzekera mpikisanowu koma Malawi inayimitsa kaye m'bindikiro wake masiku awiri apitawa.
Mpikisanowu tsopano ukuyembekezeka kudzayamba pa 25 July mpaka pa 16 August 2026 mdziko la Morocco lomwelo.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores